ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:
Yohane 4:43 - Buku Lopatulika Koma atapita masiku awiriwo anachoka komweko kunka ku Galileya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma atapita masiku awiriwo anachoka komweko kunka ku Galileya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atapita masiku aŵiriwo, Yesu adachoka napita ku Galileya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patatha masiku awiri Iye anachoka napita ku Galileya. |
ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:
Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).
Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.
Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa mu Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala mu Kapernao.
Ndipo ndinena kuti Khristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,