Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:
Yohane 4:39 - Buku Lopatulika Ndipo m'mzinda muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mudzi muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asamariya ambiri a m'mudzi muja adakhulupirira Yesu chifukwa cha umboni wa mai uja, wakuti, “Iye wandiwuza zonse zimene ndidachita.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Asamariya ambiri ochokera mʼmudziwo anakhulupirira Iye chifukwa cha umboni wa mayiyo wakuti, “Iye anandiwuza ine zonse ndinazichita.” |
Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo:
Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye.
Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?
Ine ndinatuma inu kukamweta chimene simunagwirirapo ntchito: ena anagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yao.
Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri.
ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu.
Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;