Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.
Yohane 4:31 - Buku Lopatulika Pa mphindikati iyi ophunzira ake anampempha Iye, ndi kunena, Rabi, idyani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pa mphindikati iyi ophunzira ake anampempha Iye, ndi kunena, Rabi, idyani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi imeneyo ophunzira ake a Yesu ankamupempha kuti, “Aphunzitsi, idyani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, “Rabi idyani.” |
Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.
Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.
Koma Yesu anacheuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna chiyani? Ndipo anati kwa Iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?
Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?
Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.
Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.
Ndipo pamene anampeza Iye tsidya lina la nyanja, anati kwa Iye, Rabi, munadza kuno liti?
Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona?