Yohane 4:30 - Buku Lopatulika Anatuluka iwo m'mzinda ndipo analinkudza kwa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anatuluka iwo m'mudzi ndipo analinkudza kwa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo anthuwo adatuluka m'mudzimo kubwera kwa Yesu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anatuluka mʼmudziwo ndi kupita kumene kunali Iye. |
Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga?
Ndipo m'mzinda muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita.
Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.
Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.
Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;