Yohane 4:29 - Buku Lopatulika Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tiyeni, mukaone munthu amene wandiwuza zonse zimene ine ndidachita. Kodi ameneyu sangakhale Mpulumutsi wolonjezedwa uja kapena?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tiyeni mukaone munthu amene wandiwuza ine zilizonse zimene ndinazichita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu?” |
Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.
Ndipo m'mzinda muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita.
Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo?
Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?
Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.
Ndipo Samuele anayankha Saulo nati, Ine ndine mlauliyo. Kwera, batsogola kumsanje, pakuti mudzadya ndi ine lero; ndipo m'mawa ndidzakulola upite, ndi kukudziwitsa zonse zili mumtima mwako.