Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.
Yohane 4:27 - Buku Lopatulika Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi yomweyo ophunzira ake a Yesu adafika, ndipo ankadabwa kuti Iye akucheza ndi mkazi. Komabe panalibe amene adamufunsa kuti, “Zakhala bwanji?” Kapena kuti, “Bwanji mukulankhula naye?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa nthawi yomweyo ophunzira ake anabwerera ndipo anadabwa kupeza Iye akuyankhula ndi mayi. Koma palibe amene anamufunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” kapena, “Nʼchifukwa chiyani mukuyankhula naye?” |
Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.
Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.