Yohane 4:26 - Buku Lopatulika Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuuza kuti, “Ndine amene, Ineyo amene ndikulankhula nanu, mai.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anamuwuza kuti, “Amene ndikukuyankhulane, ndine amene.” |
Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?
Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba adzakhala akuthungo.
Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene.
Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu.
Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.