Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.
Yohane 4:20 - Buku Lopatulika Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Makolo athu ankapembedza Mulungu pa phiri ili, koma inu Ayuda mumati ndi ku Yerusalemu kumene anthu ayenera kumakapembedzerako.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.” |
Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.
Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'mwamba ndi moto paguwa la nsembe yopsereza.
Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele.
Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.
Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomoni usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe.
Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza.
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?
Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake?
Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m'dziko limene munkako kulilandira, munene mdalitso paphiri la Gerizimu, ndi temberero paphiri la Ebala.
Aimirire awa paphiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordani: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.