Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Yohane 4:18 - Buku Lopatulika pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zoona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zoona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja mwakwatiwapo kale ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye tsopano si wanunso. Mwanenazi nzoona.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoona nʼzakuti iwe wakhala pa banja ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si wako. Zimene wanenazi ndi zoona.” |
Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.
Ndithu monga mkazi achokera mwamuna wake monyenga, chomwecho mwachita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israele, ati Yehova.
Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;
Mkazi anayankha nati kwa Iye, Ndilibe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndilibe;
Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino.