Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Yohane 4:15 - Buku Lopatulika Mkaziyo ananena kwa Iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mkaziyo ananena kwa Iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maiyo adati, “Bambo, patsaniko ineyo madzi amenewo kuti ndisamamvenso ludzu kapena kumadzatunganso madzi kuno.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mayiyo anati kwa Iye, “Ambuye, patseni madzi amenewo kuti ndisadzamvenso ludzu ndi kumabwerabe kuno kudzatunga madzi.” |
Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.
Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.
Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:
Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.
Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.
Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.