Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.
Yohane 4:13 - Buku Lopatulika Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Munthu aliyense womwako madzi aŵa, adzamvanso ludzu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Aliyense amene amamwa madzi awa amamvanso ludzu, |
Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.
Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake?
koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.