Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano.
Yohane 4:12 - Buku Lopatulika Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yakobe, kholo lathu ndiye adatipatsa chitsimechi, chimene mwiniwakeyo ankamwapo pamodzi ndi ana ake, ndiponso zoŵeta zake. Kodi Inu mungapambane iyeyo?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?” |
Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano.
Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti mu Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu.
Chifukwa chake anadza kumzinda wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe;
ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.
Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?
Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi.