Yohane 3:8 - Buku Lopatulika Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mphepo imaombera komwe ikufuna, ndipo umamva kuwomba kwake, koma sudziŵa komwe yachokera kapena komwe ikupita. Nchimodzimodzi munthu aliyense amene abadwa mwa Mzimu Woyera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.” |
Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake.
Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake.
Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kuchokera kumphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.
amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.
Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.
Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.