Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Yohane 3:28 - Buku Lopatulika Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Khristu, koma kuti ndili wotumidwa m'tsogolo mwake mwa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Khristu, koma kuti ndili wotumidwa m'tsogolo mwake mwa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu nomwe ndinu mboni zanga kuti ndidati, ‘Sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja, koma ndine wotumidwa patsogolo pake.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inuyo ndinu mboni zanga kuti ine ndinati, ‘Ine sindine Khristu koma ndatumidwa patsogolo pa Iye.’ |
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.
Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.
Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.
Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?