Yohane 3:26 - Buku Lopatulika Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho ophunzirawo adadza kwa Yohane namuuza kuti, “Aphunzitsi onanitu, munthu uja amene anali ndi inu patsidya pa Yordani, yemwe uja munkamuchitira umboniyu, nayenso akubatiza, ndipo anthu onse akuthamangira kwa Iye.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anabwera kwa Yohane anati, “Rabi, munthu uja munali naye mbali inayo ya mu mtsinje wa Yorodani, amene munamuchitira umboni, taonani naye akubatizanso, ndipo aliyense akupita kwa Iye.” |
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.
Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.
Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.
Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.
Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.
Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane