Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.
Yohane 3:24 - Buku Lopatulika Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo nkuti Yohane asanaponyedwe m'ndende. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (Apa nʼkuti Yohane asanatsekeredwe mʼndende). |
Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo.
Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.
Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.