Yohane 3:21 - Buku Lopatulika Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma wochita zokhulupirika amaonekera poyera, ndipo zochita zake zimadziŵika kuti wazichita momvera Mulungu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.” |
Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.
Efuremu adzati, Ndili ndi chiyaninso ndi mafano? Ndayankha, ndidzampenyerera; ndili ngati mtengo wamlombwa wabiriwiri; zipatso zako zipezeka zochokera kwa Ine.
Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!
Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.
Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;
Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.
Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.
odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko.
pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.
akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;
Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi;
Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuone Mulungu.
Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha.