Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya.
Yohane 3:20 - Buku Lopatulika Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aliyense wochita zoipa, amadana ndi kuŵala. Saonekera poyera, kuwopa kuti zochita zakezo zingaonekere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. |
Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya.
Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.
Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndili m'tulo, namuika m'mfukato mwake, naika mwana wake wakufa m'mfukato mwanga.
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.
Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.
Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.