Yohane 3:19 - Buku Lopatulika Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mlandu wake ndi uwu wakuti ngakhale kuŵala kudadza pansi pano, anthu adakonda mdima, osati kuŵalako, chifukwa zochita zao zinali zoipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. |
ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati pali chotupa choyera pakhungu, ndipo chasanduliza tsitsi likhale loyera, ndipo pachotupa pali mnofu wofiira,
Ili ndi tchimo la Ejipito, ndi tchimo la amitundu onse osakwerako kusunga chikondwerero cha Misasa.
Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonze, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.
Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.
Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?
Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.
Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.
Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.
amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.
koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,
kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirire choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.
Ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa. Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.
ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,