Yohane 21:9 - Buku Lopatulika Ndipo pamene anatulukira pamtunda, anapenya moto wamakala pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene anatulukira pamtunda, anapenya moto wamakala pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene adafika pa mtunda, adaonapo moto wamakala, pali nsomba, ndiponso buledi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi. |
ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali.
Koma akapolo anyamata analikuimirirako, atasonkha moto wamakala; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto.
Koma ophunzira ena anadza m'kangalawa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo.
Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.
Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zikwanira bwanji ambiri otere?