Yohane 21:6 - Buku Lopatulika Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵauza kuti, “Ponyani khoka ku dzanja lamanja la chombo, mupha kanthu.” Iwo adaponyadi, ndipo sadathe kulikokanso chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba. |
Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.
ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.
Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.
Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.