Yohane 21:4 - Buku Lopatulika Koma pakuyamba kucha, Yesu anaimirira pambali pa nyanja, komatu ophunzirawo sanadziwe kuti ndiye Yesu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pakuyamba kucha, Yesu anaimirira pambali pa nyanja, komatu ophunzirawo sanadziwa kuti ndiye Yesu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kutacha Yesu adaimirira pa mtunda. Komabe ophunzira aja sadazindikire kuti ndi Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu. |
Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m'maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumidzi.
Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera.
M'mene adanena izi, anacheuka m'mbuyo, naona Yesu ali chilili, ndipo sanadziwe kuti ndiye Yesu.