Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno?
Yohane 21:10 - Buku Lopatulika Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adaŵauza kuti, “Bwera nazoni nsomba zina zimene mwapha.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anawawuza kuti, “Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo.” |
Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno?
Chifukwa chake Simoni Petro anakwera m'ngalawa nakokera khoka kumtunda lodzala ndi nsomba zazikulu, zana limodzi, ndi makumi asanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinachuluka kotere, kokha silinang'ambika.
Ndipo pamene anatulukira pamtunda, anapenya moto wamakala pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate.
Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna.
Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zikwanira bwanji ambiri otere?