Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
Yohane 20:8 - Buku Lopatulika Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adaloŵa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pomaliza wophunzira winayo, amene anafika ku manda moyambirira, analowanso mʼkati, iye anaona ndi kukhulupirira. |
Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
Yesu anayankha nati kwa iye, Chifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzaona zoposa izi.
Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira.
Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaone.
Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;