Yohane 20:7 - Buku Lopatulika ndi mlezo, umene unali pamutu pake, wosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi mlezo, umene unali pamutu pake, wosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndiponso kansalu kamene kanali kumutu kwake. Kansaluko sikanali pamodzi ndi nsalu zina zija, koma padera pakokha, kali chipindire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pamodzinso ndi nsalu imene anakulungira nayo mutu wa Yesu. Nsaluyi inali yopindidwa pa yokha yosiyanitsidwa ndi inayo. |
Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.
Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsalu zabafuta zitakhala,