Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.
Yohane 20:5 - Buku Lopatulika ndipo m'mene anawerama chosuzumira anaona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sanalowemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo m'mene anawerama chosuzumira anaona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaŵerama naona nsalu zija zili chikhalire, koma iye sadaloŵemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mmene anawerama nasuzumira mʼkati mwa manda anaona nsalu zili potero koma sanalowemo. |
Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.
Koma Maria analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama chisuzumirire kumanda;
Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda;
Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsalu zabafuta zitakhala,