Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange. Iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kuchigwa, napitirira Mkusi.
Yohane 20:4 - Buku Lopatulika Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onse aŵiri adathamanga pamodzi, koma wophunzira wina uja adathamanga kopambana Petro, nkuyambira ndiye kufika kumandako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onse awiri anathamanga pamodzi koma wophunzira winayo anamupitirira Petro, nafika ku manda moyambirira. |
Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange. Iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kuchigwa, napitirira Mkusi.
wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndevu.
Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira.
Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.
Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.