Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 2:21 - Buku Lopatulika

Koma Iye analikunena za Kachisi wa thupi lake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma Iye analikunena za Kachisi wa thupi lake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma Yesu ankanena za thupi lake mophiphiritsa, pamene adaatchula Nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake.

Onani mutuwo



Yohane 2:21
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena.


Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?


Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.


Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.


Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire,


pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi,


Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.