Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 2:20 - Buku Lopatulika

Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi chimodzi analimkumanga Kachisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi chimodzi analimkumanga Kachisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Apo iwo adati, “Nyumba ya Mulunguyi idatenga zaka 46 kuti aimange, tsono Inu nkuimanga masiku atatu chabe?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?”

Onani mutuwo



Yohane 2:20
6 Mawu Ofanana  

Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.


Pamenepo anadza Sezibazara yemweyo namanga maziko a nyumba ya Mulungu ili mu Yerusalemu; ndipo kuyambira pomwepo kufikira tsopano ilinkumangidwa, koma siinatsirizike.


Ndipo Yesu anatuluka ku Kachisi; ndipo ophunzira ake anadza kudzamuonetsa chimangidwe cha Kachisiyo.


Ndipo pamene ena analikunena za Kachisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati Iye,


Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani?


ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;