Yohane 2:17 - Buku Lopatulika Ophunzira ake anakumbukira kuti kunalembedwa, Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ophunzira ake anakumbukira kuti kunalembedwa, Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira ake adakumbukira Malembo aja akuti, “Changu chomwe ndimachitira nyumba yanu chidzandiphetsa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.” |
Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya; ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.
Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena.