Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 2:14 - Buku Lopatulika

Ndipo anapeza mu Kachisi iwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anapeza m'Kachisi iwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kumeneko adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu napezamo anthu akugulitsa ng'ombe, nkhosa ndi nkhunda. Munalinso anthu osinthitsa ndalama.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo.

Onani mutuwo



Yohane 2:14
8 Mawu Ofanana  

Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa zikondwerero zake zoikika, momwemo mizinda yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa mu Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda mu Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.


Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anatulutsa onse mu Kachisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome;