Ndipo ndinaipidwa nacho kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwachotsa m'chipindamo.
Yohane 2:13 - Buku Lopatulika Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Itayandikira nthaŵi ya Paska, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu. |
Ndipo ndinaipidwa nacho kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwachotsa m'chipindamo.
Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;
Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa mu Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda mu Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;
Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka kuminda, asanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha.
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.
Koma pamene anali mu Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi.
Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;