Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.
Yohane 19:25 - Buku Lopatulika Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pafupi ndi mtanda wa Yesu padaaimirira amai ake, ndi mbale wa amai akewo, Maria mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa ku Magadala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. |
Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.
Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.
eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe.
Ndipo omdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, anaima kutali, naona zinthu izi.
Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lake Kleopa, anayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo mu Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano?
ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,
Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda.