Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.
Yohane 19:14 - Buku Lopatulika Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Paska, ndipo nkuti nthaŵi ili ngati 12 koloko masana. Pilato adauza Ayuda kuti, “Nayitu Mfumu yanu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Linali tsiku lokonzekera Sabata la Paska ndipo nthawi inali ora lachisanu ndi chimodzi masana. Pilato anati kwa Ayuda, “Nayi mfumu yanu.” |
Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.
Ndipo m'mawa mwake, ndilo tsiku lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhana kwa Pilato,
Ndipo ora lake pamenepo linali ngati lachisanu ndi chimodzi. Ndipo panali mdima padziko lonse kufikira ora lachisanu ndi chinai, ndipo dzuwa linada.
Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi.
Pamenepo Yesu anatuluka kunja, atavala korona waminga, ndi malaya achibakuwa. Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu!