Yohane 19:1 - Buku Lopatulika Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Pilato adalamula kuti atenge Yesu ndi kumkwapula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Pilato anatenga Yesu namukwapula mwankhanza. |
Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.
Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.
nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.
Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina;
Koma anakakamiza ndi mau okweza, napempha kuti Iye apachikidwe. Ndipo mau ao anapambana.
kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende;
amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.