Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.
Yohane 18:9 - Buku Lopatulika kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataye mmodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataya mmodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa (Adaatero kuti zipherezere zimene Iye adaanena kale kuti, “Sindidatayepo ndi mmodzi yemwe mwa amene mudandipatsa.”) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Izi zinachitika kuti mawu amene Iye anayankhula akwaniritsidwe: “Ine sindinataye ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene mwandipatsa.” |
Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.
Koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi ichi, kuti za ichi chonse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndichiukitse tsiku lomaliza.