Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye paguwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.
Yohane 18:12 - Buku Lopatulika Ndipo khamulo ndi kapitao wamkulu, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga Iye, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo khamulo ndi kapitao wamkulu, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga Iye, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Gulu la asilikali achiroma lija, pamodzi ndi mtsogoleri wao, ndiponso asilikali achiyuda, adagwira Yesu nammanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka gulu la asilikali ndi olamulira wawo ndi akuluakulu a Ayuda anamugwira Yesu. Iwo anamumanga. |
Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye paguwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.
Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe.
Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.
Ndipo iwo akugwira Yesu ananka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe.
Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse.
Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe aakulu onse ndi akulu a anthu, ndi alembi.
Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.
Ndipo pamenepo anamgwira Iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutali.
Pamenepo Yudasi, m'mene adatenga gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe aakulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida.
Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,
Ndipo m'mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkulu wa gululo kuti mu Yerusalemu monse muli piringupiringu.
Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki?
Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga.
Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m'kaidi.