Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.
Yohane 18:10 - Buku Lopatulika Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lake lamanja. Koma dzina lake la kapoloyo ndiye Malkusi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lake lamanja. Koma dzina lake la kapoloyo ndiye Malkusi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Simoni Petro anali ndi lupanga. Adalisolola, natema kapolo wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Kapoloyo dzina lake anali Malkusi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi). |
Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.
Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lake, nakantha kapolo wake wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake.
Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe ndiye mbale wake uja amene Petro anamdula khutu, ananena, Ine sindinakuone iwe kodi m'munda pamodzi ndi Iye?