Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.
Yohane 17:13 - Buku Lopatulika Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo okha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo okha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tsopano ndilikudza kwa Inu. Ndikulankhula zimenezi pamene ndili pansi pano, kuti chimwemwe changa chikhalenso chodzaza mwa iwowo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. |
Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.
Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.
Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu,
Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife.
Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.
Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndili ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine.
Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire.