Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.
Yohane 16:9 - Buku Lopatulika za machimo, chifukwa sakhulupirira Ine; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 za machimo, chifukwa sakhulupirira Ine; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngolakwa pa za kuchimwa, chifukwa sandikhulupirira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine. |
Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.
Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro;
Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.
ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;
Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;