Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wake kufikira mapazi ake, monga momwe apenyera wansembe;
Yohane 16:8 - Buku Lopatulika Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Iyeyu atafika, adzaŵatsimikiza anthu a pansi pano kuti ngolakwa pa za kuchimwa, za kulungama, ndiponso za kuweruza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo. |
Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wake kufikira mapazi ake, monga momwe apenyera wansembe;
Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.
Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.
Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji?
Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati.
Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?
Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;
kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.