Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 16:18 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake ananena. Ichi nchiyani chimene anena, Kanthawi? Sitidziwa chimene alankhula.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake ananena. Ichi nchiyani chimene anena, Kanthawi? Sitidziwa chimene alankhula.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kodi nchiyani akunenachi kuti, ‘Kanthaŵi pang'ono?’ Sitikumvetsa zimene akufuna kunena.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”

Onani mutuwo



Yohane 16:18
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!


Mwa ophunzira ake tsono anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundione; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, chifukwa ndimuka kwa Atate?


Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa Iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzake za ichi, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine?


Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.