Yohane 16:12 - Buku Lopatulika Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ndili nawo mau ena ambiri oti ndikuuzeni, koma simungathe kuŵamvetsa tsopano ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndili ndi zambiri zoti ndiyankhule nanu, koma simungathe kuzilandira tsopano. |
Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;
Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.
Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani.
kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;