Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima; m'mwemo aona nkhope yake mokondwera; ndipo ambwezera munthu chilungamo chake.
Yohane 14:8 - Buku Lopatulika Filipo ananena ndi Iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo chitikwanira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Filipo ananena ndi Iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo chitikwanira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Filipo adati, “Ambuye, tiwonetseni Atatewo, mukatero tikhutira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Filipo anati, “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo ife tikhutitsidwa.” |
Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima; m'mwemo aona nkhope yake mokondwera; ndipo ambwezera munthu chilungamo chake.
Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.
Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.