Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.
Yohane 13:30 - Buku Lopatulika Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anatuluka pomwepo. Koma kunali usiku. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anatuluka pomwepo. Koma kunali usiku. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yudasi atalandira mkate uja, pompo adatuluka. Nthaŵiyo nkuti kutada kale. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yomweyo Yudasi atangodya buledi, anatuluka, ndipo unali usiku. |
Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.
Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosachimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi chipasuko zili m'njira mwao.
Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.
Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote.