Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.
Yohane 13:29 - Buku Lopatulika Pakuti popeza Yudasi anali nalo thumba, ena analikuyesa kuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa pachikondwerero; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti popeza Yudasi anali nalo thumba, ena analikuyesa kuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa pachikondwerero; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popeza kuti Yudasi ankasunga thumba la ndalama, anzake ankayesa kuti Yesu akumuuza kuti, “Kagule zofunika paphwando pano,” kapena kuti akapereke kanthu kwa osauka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka. |
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.
Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.