Ndipo anaona Yakobo kuti mu Ejipito munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake aamuna, Chifukwa chanji mulinkuyang'anana?
Yohane 13:22 - Buku Lopatulika Ophunzira analikupenyana wina kwa mnzake, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ophunzira analikupenyana wina kwa mnzake, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira aja adayamba kupenyetsetsana, osadziŵa konse kuti akunena yani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira ake anapenyetsetsana wina ndi mnzake, posadziwa kuti amanena za yani. |
Ndipo anaona Yakobo kuti mu Ejipito munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake aamuna, Chifukwa chanji mulinkuyang'anana?
ndipo m'mene analinkudya, Iye anati, Indetu ndinena kwa inu, mmodzi wa inu adzandipereka Ine.
Ndipo iwo anagwidwa ndi chisoni chachikulu, nayamba kunena kwa Iye mmodzimmodzi, Kodi ndine, Ambuye?
Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.
Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.
Yesu m'mene adanena izi, anavutika mumzimu, nachita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.