Tchulani zinthu zimene zilinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, chitani zabwino, kapena chitani zoipa, kuti ife tiopsedwe, ndi kuona pamodzi.
Yohane 13:19 - Buku Lopatulika Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikukuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire kuti Ine ndinedi Ndilipo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ine ndikukuwuzani tsopano zisanachitike zimenezi, kuti pamene zachitika, mudzakhulupirire kuti Ine Ndine. |
Tchulani zinthu zimene zilinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, chitani zabwino, kapena chitani zoipa, kuti ife tiopsedwe, ndi kuona pamodzi.
Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.
chifukwa chake ndinakudziwitsa ichi kuyambira kale; chisanaoneke ndinakusonyeza icho, kuti iwe unganene, Fano langa lachita izo, ndi chifaniziro changa chosema, ndi chifaniziro changa choyenga zinazilamulira.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.
Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanene kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.
Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.
Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.