Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.
Yohane 13:16 - Buku Lopatulika Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kunena zoona, wantchito saposa mbuye wake, nthumwinso siiposa woituma. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. |
Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.
Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso.
Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.
Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.
Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.
Koma ndinayesa nkofunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa;