Yohane 13:12 - Buku Lopatulika Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu? |
Momwemo Ezekiele adzakhala kwa inu chizindikiro; umo monse anachitira iye mudzachita ndinu; chikadza ichi mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
Pakuti wamkulu ndani, iye wakuseama pachakudya kapena wakutumikirapo? Si ndiye wakuseama pachakudya kodi? Koma Ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira.
ananyamuka pamgonero, navula malaya ake; ndipo m'mene adatenga chopukutira, anadzimanga m'chuuno.
Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwake.